27/09/2026
🛑 TIKAMBEKO ZA MASAMBA A MA GWAVA (GUAVA LEAVES) 🛑
Mwaswela bwanji ENIKHOMO...? Nanga tsiku linali bwanji..?
Madzulo ano, Tiyeni tioneko zokhudza masamba a ma gwava.
Ambiri mwaife mmakomomu tili ndi mitengo imeneyi yosawelengeka koma timangodziwa k*tafuna zipatso zake ndipo samadya mkomwe and masamba akewo amangowathira pansi kapena kuwatentha popanda kudziwa mphamvu ndi kufunika kwake. Dziwani k*ti Masamba amenewa ndi Dhilu, Makolo athu ankawagwiritsa ntchito kwambiri pochiza matenda osiyanasiyana. Chonde Werengani mpaka kumapeto, kenako SHARE with others ♥️ k*ti anzanu nawonso apindule.
✨️MAUBWINO AKE:
🍀 Masamba a gwava amathandiza kuletsa k*tsegula m'mimba (diarrhea): Mmasamba amenewa amakhala ndi ma Natural chemicals otchedwa tannins othandiza kupha mabakiteriya m'mimba ndikulimbitsa mmene mimba imagwirira ntchito kumbali imeneyi ya chimbuzi.
🍀Masambawa Amathandiza kuchepetsa ululu wa mano ndi k*tupa kwa misempha ya mano mmaGums, k*tafuna tsamba limodzi lopuk*tidwa bwino kumapha mabakiteriya opangitsa ululu umenewu.
🍀 Amathandizanso kuwongolera shuga m'magazi (Balance): kumwa tea wa masamba a magwava pafupipafupi kumathandiza anthu odwala shuga (diabetes) kukhala ndi mlingo wa sugar oyenera.
🍀 Amathandizanso kuchepetsa cholesterol oyipa m'magazi, zomwe zimathandiza mtima kukhala wathanzi.
🍀 Azimayi amagwiritsanso ntchito madzi a masamba a gwava k*tsuka pamalo poberek.ra pambuyo pa kubereka, izi zimathandiza kuchira msanga ndi kupewa matenda pa balapo.
💥 REMEDY YAKE:
Tengani masamba a gwava aawisi khumi, tsukani bwino bwino, phikani m'madzi okwana 500ml kwa mphindi 10-15. Sefani mu ka sefa, mumwe zotentha pang'ono, maulendo awiri patsiku (m'mawa ndi madzulo) kwa masiku atatu ngati muli ndi Diarrhea. Ku mano opweteka, mudzingotafuna tsamba limodzi nthawi inayake maka mukamava ululu.
⚠️ Ngati k*tsegula mmimba kukupitirira masiku atatu kapena mukuchita mwa magazi, kapena mowirikiza kwambiri pitani kuchipatala msanga musangodalira remedy yokhayi.
_________________
🌳Osaiwala Nanunso k*tigaila zomwe mudziwa ngati mudayamba mwagwiritsapo ntchito masamba a gwava.
Osaiwalanso kupanga LIKE....SHARE...Zikomo